Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 221
Matigari
wanenayotu ndi yolondola."
"Pali kusiyana kwakukulu pakati pa anthu ndi zinyama,"
Guthera anawonjezera mosonyeza kuti akuganizira zinazake.
"Anthu akhoza kusunga chakudya munkhokwe ndipo ngati
atachita zimenezi chakudya chikayamba kusowa sangama-
khaule ndi njala. Zimenezitu zikutanthauza kuti anthu aka-
mavutika ndi njala amakhala kuti achita kufuna."
Matigari anayang'ananso Guthera mokhala ngati sanayambe
wamuonapo.
"Zimene ukunenazitu ndi zoona zenizeni." anabwerezanso
Matigari.
"Vuto ndi lakuti zinthu zonse zimene anthu ambiri amapeza
zimalowa m'matumba a nthata zoyamwa anzawo magazi. Ama-
gulitsa chakudya chonse n'cholinga choti maakaunti awo aku-
banki asefukire ndi ndalama. Ndithudi abale, ndodo ya chitsiru
ndi imene munthu wochenjera amathyolera mango chitsirucho
chikusakasaka miyala yogendera mangowo," anatero Guthera.
"Panopa ndi pamene ndamvetsa chimene mwakhala muku-
chimenyera nkhondo kwa zaka zonsezi. Simukufuna kukhala
ngati chitsiru. Simukufuna kumawedza nsomba n’kuika mum-
tanga kuti nthata zoyamwa ena magazi zizibwera n’kukuwedze-
rani mumtangamo!"
Anthu anali m'galimoto aja sanatsikebe. Kenako Matigari
anaitana Muriuki:
"Achimwene, basi tsikani mumtengomo."
Muriuki anatsikadi n'kupita pamene panali Matigari ndi
Guthera.
"Ndikufuna ndikutume. Uyende molowera kumene kuli gal-
imotoyo ndipo uziyerekezera kuti ndiwe m'busa wang'ombe
220