Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 220

Matigari Gawo 14 "Ndiye kuti nsewu tinaoloka uja suli kutali?" Guthera ana- funsa. "Muriuki, takwera mumtengowu uone kuti ndi ndani," Matigari anatero. Muriuki anakwera mumtengo muja. Kunalibe nsewu pafupi. Koma zinali zoonadi kuti ankaona galimoto. Galimotoyo inkayenda ngati nkhono. Kenako inaima pafupi ndi ziyango- yango zina chapataliko pang'ono ndi pamene anaimapo. "Ndi Mercedes-Benz! Mercedes-Benz!" Muriuki anakuwa. "Koma tsopano yaima." Matigari ndi Guthera anachoka pachigompholera chimene anabisala. Kenako anayamba kuyang'ana kumene kunali galimo- to kuja. Inalidi galimoto yakuda yamtundu wa Mercedes-Benz. Kenako anayamba kudikirira kuti amene anali m'galimotomo atuluke. Chapatali pang'ono kuchokera kumene kunali galimotoyo kunali gulu la nkhosa komanso ng'ombe. Kupatulapo zinthu zimenezi, m'chigwacho munalibenso chilichonse ndipo ukayan- g'ana mbali zonse, chigwacho chinkakhala ngati chilibe malire. "Kodi ziweto zimenezi zikudya chiyani padzuwa ngati pamenepa?" Guthera anafunsa, akuloza kumene kunali nkhosa ndi ng'ombe kuja. "Mkaka umachokera kung'ombe, ndipo ng'ombe zimadya nsipu. Choncho ngati nyama zilibe chakudya ndiye kuti anthun- so asowa mkaka woti amwe. Choncho ngati ndafunsa za ng'ombe, ndiye kuti ndikunenanso za abusa oweta ng'ombezo." Matigari anayang'ana Guthera n'kunena kuti, "Mfundo 219