Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 218
Matigari
Koma kungoyambira dzulo pamene ndinaphwanya lamulo
langa la khumi ndi chimodzi, ndinayamba kusankha ndekha zo-
chita. Ndikanatha kusankha kuchita zimenezo kapena ayi. Ko-
ma ndinachita kufuna ndekha kuti zimene ndimafuna zitheke."
"Koma sikuti zimenezi ndi zimene ndikufuna ndikuuzeni.
Ndakhala ndikudziwa kuti moyo umene ndimakhala m'mbuy-
omu unali ngati wachinyama. Moyo wanga sunali wosiyana
mpang'ono pomwe ndi wanyama yakutchire yomwe imapuma,
kudya, kumwa kenako n'kupita kukagona kwinaku ikudikirira
tsiku lakufa. Chimene ndikunenera zimenezi si kokha chifukwa
choti ndazindikira kuti ndakhala ndikukhala moyo wopanda
cholinga chenicheni m'mbuyomu. Ndikudziwa kuti palibe mzi-
mayi amene sadziwa mavuto osaneneka amene azimayife tima-
kumana nawo."
"Chomwe chikundisowetsa mtendere ndi ichi: Munthu
akadziwa zoyenera kuchita, kodi amangokhala n'kupinda manja
ake? Kodi kungodziwa zinazake ndi kokwanira? Kodi ndi zo-
kwanira kuti ndingonena kuti tsopano ndazindikira? Ndikufuna
kuchita chilichonse chomwe ndingathe kuti ndichotse zinthu
zimene zikuchititsa kuti anthu azikhala moyo ngati zinyama,
makamaka azimayi. Kodi palibe chilichonse chimene azimayife
tingachite kuti tisinthe zinthu pamoyo wathu? Kapena tingopi-
tiriza kutsatira njira imene amuna atipangira, kuti basi amuna
azingowongolera moyo wathu? Kodi mesa m'dziko muno ambi-
ri ndi azimayi? Tiyeni tizipita! Kuyambira lero ndikufuna
ndikhale mayi woyambirira kumenyera ufulu wathu. Sindilola
kuti ndizingokhala kumbuyo nthawi zonse. Matigari,
yendetsani miyendo yanu kuti zipolopolo zilire ngindee!
217