Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 215
Matigari
ngati agalu komanso akhwangwala? Ndikukuuzani, Boy
andimva madzi ndipo sadzagonanso m'nyumba yomanga ine!"
"Ndiye tingoyerekeza kuti akugwirani n'kukumangani,
mwina kukupititsani kundende kapena kuchipatala cha amisa-
la? Kodi mukuganiza kuti angokusiyasiyani, akhozatu kuku-
phani!"
"Tadikira ndikuuze chinthu chimodzi," Matigari anatero.
“Kaya akanditsekera kundende, kaya andipha, anthu omwe
amapindula chifukwa cha khama lathuwa sangakwanitse kutse-
ka pakamwa munthu aliyense. Ndikukuuza kuti sipadzakhala
mtendere pakati pa anthu omwe amachita khama kugwira
ntchito, ndi nthata zomwe zimangoyamwa ena magazi. Mtende-
re, mgwirizano kapena chikondi sizidzakhalapo ata!
Sizingatheke zimenezo! Tangoyerekezera kuti makolo athu
ankachita zinthu ngati alibe maso kuti aone, alibe makutu kuti
amve, kapena alibe lilime kuti ayankhule? Kodi bwenzi lero tili
pati? Dzulodzuloli, ndikutitu dzulo, ndimaganiza kuti ngati
nditadzimanga lamba wamtendere ndipeza choonadi komanso
chilungamo m'dzikoli. Chifukwa ena amati choonadi ndi chi-
lungamo ndi zamphamvu kwambiri kuposa lupanga. Amati
mdani amene watulutsidwa mwamtendere, pochita kukambira-
na, samabwereranso. Koma amene wachita kuthamangitsidwa
ndi zikwanje amabweranso. Koma kodi maganizo amenewa an-
difikitsa kuti? Choyamba kundende, kenako kuchipatala cha an-
thu amisala. Zikanakhala kuti inu simunandithandize, kodi
bwenzi ndili kuti lero? Bwenzi ndidakali kundende kapena ku-
chipatala cha amisala. Bwenzi nditawolera komweko. Kungo-
yambira dzulo, ndaphunzira kanthu kena kofunika kwambiri.
Mwina ndinene kuti ndaphunzira phunziro latsopano komanso
lakalekale. Mdani sangathamangitsidwe ndi mawu okha,
214