Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 214

Matigari "Tikupita kunyumba!" Matigari anamuyankha. Muriuki ndi Guthera anayang'anizana. Iwo ankadzifunsa kuti, zoona akufunabe kupita kunyumba yomwe yamulowetsa m'mavuto onsewa? "Kodi simukuona kuti ndi bwino kungowasiya anthu ame- newa?" Guthera anafunsa. "Kodi ino si nthawi yabwino yongosi- ya kufunsa mafunso ambirimbiri? Mungachitetu bwino kungoiwala za nyumba yanuyo n'kupulumutsa moyo wanu! Ingomatani milomo yanuyo basi!" "Kodi ukutanthauza kuti ndimate moyo wanga n'kuuponya m'manda? Ukutanthauza kuti ndisiye zonse zomwe ndina- zikhetsera thukuta, zomwe ndinazimanga ndi manja anga? Ndisiyire chilichonse nthata zoyamwa ena magazizi? Tamvet- sera Guthera. Dzikolitu lazondoka, koma ineyo ndikufuna ndili- tembenuze. Ineyo ndaona kuti m'dziko lathuli mabodza ndi amene amaonedwa kuti ndiye zolondola, ndipo zolondola ndi zimene zimaoneka kuti ndiye mabodza. Umbava komanso mchitidwe waziphuphu zangosanduka mbali ya moyo wa tsiku ndi tsiku, moti kuchita zosiyana ndi zimenezi ukumakhala ngati wapenga. Anthu akumapatsana ziphuphu mochita kunyadirira masiku ano. Kodi n'zoona kuti abusa asiye nkhosa zawo m’man- ja mwa mimbulu komanso afisi kuti aziziweta? Zinthu m'dzikol- idi zasokonekera, ndipo ineyo ndipita kuti ndikazikonze. Womanga akufuna malo oti azigona. Mlimi akufuna zokolola zake. Nayenso wogwira ntchito akufuna phindu la ntchito yake. Ife takana kukhala ngati mapoto omwe amaphika chakudya ko- ma osadya nawo. Kapenatu iwe ukufuna kuti azimayi athu azig- ulitsa matupi awo kuti apeze yamchere! Komanso ana athu, kodi ukufuna apitirize kutoleza m'mabini komanso kumtaya 213