Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 213
Matigari
Gawo 13
Matigari, Guthera ndi Muriuki anali atakhala pansi pa
mtengo wina kuyesa kuti apezeko kanthunzi ngakhale kuti
mtengowo unalibe masamba. Dzuwa linkawamba, kunja kunka-
tentha kuposa muuvuni ndipo linawawaula osati pang'ono.
Udzu unali utafoteratu chifukwa cha kutentha.
"Dzuwalitu ndiye likuchititsa kuti kutenthe ngati moto,
mwati sitiyamba kufuka kaya! Tikayerekezera ndi dzulo lija ler-
olo tikungokhala ngati tili m'chiwaya chomwe chili pamoto."
anatero Guthera.
"Indedi, dzulo lija nyengo yake simadziwika bwinobwino,"
anayankha motero Muriuki. "Sitinganene kuti kunja kumatentha
kapena kumazizira."
"Kutentha kumenekutu kukhoza kukudwalitsa, dzuwa ku-
wala ngati enaake alituma." anawonjezera motero Guthera.
Matigari anali atagona. Iye anagwiritsa ntchito chijasi chake
chija ngati pilo. Nkhope yake anali ataivindikira ndi chisoti
chake chija. Pa nthawiyi anaganiza zoti abeko katulo ndipo
ankaliza mkonono ngati ntchini. Guthera ndi Muriuki anali ata-
khala pansi. Guthera anali atakoleka m’khosi mwake kampango
ka mwina moyera mwina mwakuda. Zovala zimene Muriuki
anavala zinali za zigamba za mitundu yonse imene mugaigan-
izire.
"Tiyeni tiwadzutse," Guthera anatero. Koma mawu akewa
adakali m'kamwa, Matigari anadzuka.
"Tiyeni tidzipita," Matigari anatero. Mmene anayankhulira
sizinkaoneka n'komwe kuti wangodzuka kumene.
"Ndiye tikupita kuti?" anafunsa Muriuki.
212