Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 212

Matigari Gawo 12 . . . Chilengezo chapadera . . . Apolisi aulula kuti wamisala wina amene wathawa ndi uja akumadzitchula kuti Matigari ma Njiruungi. Anthu onse a m'dziko muno akuchenjezedwa kuti asamale ndi mun- thu ameneyu chifukwa ndi woopsa. Iye akumaganiza kuti chilichonse ndi chake monga nyumba, malo, mafakitale komanso ngakhale azimayi onse akuti ndi ake. Aka ndi kachiwiri kuti munthu ameneyu athawe atamangidwa. Ulendo woyamba anamangidwa pamene ankalimbana ndi a John Boy Junior pa nkhani ya malo. Iye anauza a Boy kuti akufu- na makiyi a nyumba yake ndipo ankachita zimenezi mwachiwawa. Mpaka pano sizinadziwikebe kuti anathawa bwanji kuchokera muselo limene anatsekeredwa. Kenako anagwidwa n'kupititsidwa kuchipatala cha anthu amisala dzulo pambuyo ponyoza Nduna Yoona Zachilunga- mo. Ndunayi imachititsa msonkhano wothetsa mkangano womwe unachitika pakati pa ogwira ntchito komanso oyendetsa kampani. Apolisi akufufuzabe kuti chinachitika n'chiyani kuti mzimayi komanso mnyamata wina aloledwe kulowa m'chipatalachi pataperekedwa chilengezo kuti amisalawa atsekeredwe kumalo achitetezo chokhwima. Apolisi akudikirabe mzimayi komanso mnyamatayu kuti apite kupolisi n'cholinga choti awathandize pakafukufukuyu. Apolisi ena atumizid- wa kuti apite azikalondera nyumba ya John Boy Junior . . . komanso John Boy Junior wapatsidwa asilikali omuteteza kwa Matigari ma Njiruungi . . . 211