Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 211
Matigari
Gawo 10
. . . Ino ndi Wailesi Yanu ya Choonadi . . . Apolisi auzidwa kuti asa-
mavutitse kapena kugwira azungu omwe sanamete tsitsi komanso nde-
vu zawo. Auzidwanso kuti asamawavutitse ngati avala zovala zosaon-
eka bwino, akapezeka akuimitsa galimoto kapena ngati alibe ndalama
zolipirira basi. Apolisi apereka chilengezo chimenechi boma la United
States komanso Britain litadandaula kuti anthu a m'maiko awo
akumavutitsidwa akamayenda m'misewu ya m'dziko muno chifukwa
anthu akuwaganizira kuti ndi amisala kokha chifukwa choti sanamete
ndevu kapena tsitsi lawo. Nduna Yoona Zachilungamo yapepesa mai-
kowa ndipo yachenjeza anthu onse kuti asiyiretu mtima watsankho.
Anthu onse akuchenjezedwa kuti asamapezere anthu a mitundu ina
zifukwa kokha chifukwa chakhungu lawo. Mkulu wa apolisi wauza
apolisi komanso anthu onse a m’dziko muno kuti anthu achizungu
samapenga misala, zivute zitani. Apolisi akufuna kudziwitsa aliyense
kuti anthu amene athawa kuchipatala cha amisala, kupatulapo a
m'mayiko achimwenye, onse anali anthu akuda . . .
Gawo 11
Tsopano mvetserani chilengezo china chapadera . . . Chilengezo
chapadera . . . Apolisi awombera wamisala m'modzi amene anathawa.
Apolisi apeza kuti wamisala ameneyu ndi Ngaruro wa Kiriro.
Apolisiwo anaona kuti sangachitire mwina koma kumuombera chifu-
kwa amaika miyoyo ya ena pangozi. Atamuombera anavulala kwambiri
moti anathamangira naye kuchipatala. Asanawomberedwe, anayamba
kuthupsa apolisiwo komanso amaopseza kuti ayambitsa zachiwawa.
Amanenanso kuti apitirizabe kusokoneza ogwira ntchito kuti azinyan-
yala ntchito. Wamisalayu amayesanso kusokoneza apolisiwo ndi ma-
ganizo ake oipawo powauza kuti nawonso ndi ogwira ntchito. Anawau-
zanso kuti iwowo ali ngati zidole za boma la anthu olemera, eni malo a
m’dziko muno komanso ali ngati akazitape a olamulira ankhanza . . .
210