Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 21

Matigari Bambo uja anangoima chapatali atachita tsembwe ndi zimene ankaonazo. Anadandaula kuti, “Ana angaa! Zoona ana anga?” Azibambo anaima pachipata aja anachokera limodzi ndi chigalimoto chija ndipo m’mbuyo mwawo anasiya phokoso la ana komanso nyama zomwe zinkasakasaka zinthu pamulu wa zinyalala zija. “Ndatola wailesi! Ndatola wailesi!” Mnyamata wina anafuula motero, kwinaku akulumphalumpha, chimwemwe chitadzadza tsaya. Posakhalitsa, palibe chinyalala pamulu uja chomwe chinasiidwa chosatembenuza. Mwana aliyense anali atanyamula kaphukusi kake ka zinthu. Ena anatola ulusi, makatoni, mapepala apulasitiki, mapaipi, zigamba zamitundumitundu ndi chilichonse chomwe anachiona kuti angakachigwiritse ntchito. Ena anali akutafuna tomato woola, ndipo ena ankatsopa mokhala ngati akutsukuluza mafupa a nyama omwe anatola. Kenako anaona ana awiri akukanganirana zingwe za nsapato ndipo ena anawazungulira n’kumachemerera. Pa ana amene ankamenyanawo, mwana yemwe ankaoneka wamkuluko anachipulumutsa chibakera ndipo chinafikira m’mutu mwa mnzakeyo moti chinamunyamula n’kumugwetsera pansi. Kenako wamkulu uja anambwandira khosi la mnzakeyo. Mwana anagwidwa pakhosiyo ankangophiriphitha ngati nkhuku yomwe ikutsirizika pambuyo poti aionetsa mpeni. Komabe, mwanayo sanasiye ulusi womwe unali m’manja mwake uja. Tsopano bambo uja anatola ndodo n’kuyamba kuthamangira kunali ana kuja. Mwana ankamenya mnzake uja atangomuona bamboyo, anamusiya mnzakeyo n’kuthawa ndipo anakaima 20