Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 209
Matigari
Gawo 6
Mwatsegulayi ndi Wailesi Yanu ya Choonadi . . . Tsopano mvet-
serani chilengezo chinanso chochokera kupolisi . . . Apolisi akulimbitsa
munthu aliyense amene angaone munthu amene akuyankhula ngati
wamisala kuti akanene kupolisi yapafupi. Ayenera kukanena kupolisi
akaona munthu amene wavala nsanza ngati wamisala kapena aliyense
yemwe sanamete kapena kupesa tsitsi lake. Ayeneranso kukanena ngati
ataona munthu aliyense amene akufunsa mafunso osadziwika bwino
komanso amene akuchita zinthu zomwe ndi amisala okha omwe amazi-
chita. Apolisi anena kuti aliyense yemwe si wamisala ayenera kumeta
ndevu komanso tsitsi lake komanso kumavala molongosoka nthawi
zonse. Aliyense asayerekeze, tikubwerezanso kuti asayerekeze kuyenda
munsewu atavala nsanza chifukwa akhoza kugwidwa . . .
Ndiye zinangochitika kuti pamene mayi wina wachikulire
komanso mwamuna wake ankatoleza m'mabini ena, anaona
chithunzi cha Yesu Khrisu komanso cha Karl Marx.
"Anthu odwala omwe akuwalengeza pawailesiwa kuti atha-
wa kuchipatala cha amisala aja si awa!" mayiyo anauza
mwamuna wake.
"Kukhala ngatiditu ndi omwewo! Onsewa ali ndi tsitsi lalita-
li komanso ndevu zambiri, ndipo akungooneka ngati akudwala
misala!" mwamuna uja anatero.
Onse anatenga chithunzi chimodzichimodzi n'kuthamangira
nacho kupolisi.
"Nyinyi wenda wazimu!"* wapolisi anayankhula mokalipa. " Ife
tikufuna amisala enieni, osati zithunzi ayi! Pitani mukafufuze
amisala omwe athawa kuchipatala mubwere nawo kuno,
kapena ngati mukudziwa kumene ali ingotiperekezani . . . "
208