Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 208

Matigari Gawo 4 Wansembe uja atangomva zoti amisala athawa kuchipatala, anabzala maondo ake pansi n'kuyamba kupemphera kwa Mulungu. “Oh, Ambuye. Simunandipatse mpata woti ndikayen- dere anthu omwe anali kuchipatala cha anthu amisala . . . Ndiye ngati mulidi inuyo mwabwera n'kudzionetsa kwa ife ngati mun- thu wamisala, chonde mudzakumbukire kuti mtumiki wanune ndimafuna kupita kukawaona mawamawali . . .” Gawo 5 Ino ndi Wailesi Yanu ya Choonadi . . . Chidziwitso chapadera. Apolisi akufufuza anthu ena openga omwe athawa kuchokera ku- chipatala cha anthu amisala. Apolisiwa akufunafunanso mzimayi ko- manso mnyamata wina, omwe chakum'mawa anapita kuchipatalachi kukapereka chakudya kwa odwala. Apolisi akupempha mnyamata ko- manso mayiyo kuti apite kukadzipereka kwa apolisi a m'dera limene akukhala kuti athandize apolisi kudziwa kumene anthu oopsawa ali, ko- manso kuti adziwe kuti anathawa bwanji. 207