Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 205
Matigari
Gawo 1
Iye anapanga chiganizo chake adakali kuchipatala cha anthu
amisala kuja. Ankaona kuti munthu sangagonjetse mdani wake
ndi zida zokha, koma ankaonanso kuti munthu sangagonjetse
mdani wake ndi mawu okha. Anaona kuti ayenera kukhala ndi
mawu oyenerera, komanso kuti mawuwo apatsidwe mphamvu
zokwanira bwino ndi zida zankhondo. Kuganizira mmene ana-
zunzikira kufunafuna choonadi ndi chilungamo atadzimanga
ndi lamba wamtendere kunamupangitsa kusintha maganizo.
Anaona kuti chilungamo sichingapezeke ngati munthu atatsatira
njira yochita zinthu mwamtendere. Kenako anadziuza kuti:
“Pamene wosula zitsulo ankabwerera kwawo atapita koka-
kulitsa luso lake, anapeza munthu wina akukhaulitsa mkazi
wake yemwe anali woyembekezera. Kodi akanangomupatsa
moni munthuyo mwaulemu? Ayi ndithu. Kumeneku kunali ku-
mutokosola dala. Iye anayamba kunola mpaliro wake kuti
atumbule nawo munthu ankazunza mkazi wakeyo! Inenso an-
thu amenewa sindingangowasiyasiya.”
“Anthu amene akuponderezedwa amapeza chilungamo kud-
zera mumpaliro wonoledwa bwino.” Kenako anachotsa lamba
wamtendere uja ndipo anamuponya pansi n'kuyamba kumu-
pondaponda.
204