Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 203

Matigari Gawo 19 Palibe boma lililonse, ngakhale litakhala lankhanza chotani, lomwe linakwanitsapo kuletsa zonena za khamu la anthu ambiri. Nyimbo zija zinafala paliponse ngati moto wolusa. Zinkaimbidwa m'midzi yonse. Anthu ankaimba nyimbozi usiku ndi usana. Nthawi zina ankayamba ndi nyimbo ya wophunzira uja: Ngakhale mutiphe, Chipambano ndi chathu! Chipambano ndi chathu! Kenako ankayamba kuimba nyimbo ya Matigari ma Njiruun- gi: Ndionetseni munthu Yemwe dzina lake ndi Matigari ma Njiruungi, Yemwe akamayenda m’mapazi mwake m’malira maberu. Komanso zipolopolo, ngindee! Komanso zipolopolo, ngindee! Koma kodi Matigari ma Njiruungi anali ndani kwenikweni? 202