Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Página 201

Matigari kukuwa n'kumatuluka kuchoka muholoyo ngati mbewa zobuli- ka pam’buli. Onse anayamba kubalalikira m'makwawo. Koma atangofika kwawo, ankangoyankhula nkhani ya Matigari ma Njiruungi, Ngaruro wa Kiriro komanso wophunzi- ra wanzeru wa kusukulu yaukachenjede uja. "Mwati chiyani?" anafunsa motero anthu omwe sanapiteko. "Iye ananena kuti masiku a mbava zankhanzazi komanso antchito awo atsala owerengeka." "Tsiku la 40 la mbavazi layandikira?" "Ndiyeno masiku amenewa akangotha?" "Iii, nanunso, kodi mukufuna kuti tichite kukuuzani chili- chonse?" "Abweranso. Iye sananene kuti abwera liti, koma anati abwera ndithu!" "Koma ndiye ndi zodabwitsatu! Mwati dzina lake ndi nda- ni?" "Matigari ma Njiruungi." "Ndi zoonadi. Zonse zimene anthu akhala akunena ndi zo- onadi. M'dziko munodi muli anthu a mitundu iwiri. Pali ena omwe amagulitsa dziko lawo, ndiye pali ena omwe amame- nyera nkhondo ufulu wadziko lawo." "Matigari ma Njiruungi akumenyera ufulu wadziko lathu." 200