Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 20

Matigari Ana aja anathamanga mokhala ngati akupikisana ndi chigalimoto chija mpaka anakalowa kumtaya. Malowa anali aakulu kwambiri ndipo anazunguliridwa ndi mpanda wawaya. Pampandawo panali pataima akhwangwala ndipo ena anali ali m’mitengo yomwe inali chapafupi. Nazonso ziwombankhanga zinkauluka chapatali m’mlengalenga maso awo akuthwa ali dwii kuyang’ana tianyamata toyendayenda tamiyendo inayi toti zitole. Gulu la agalu opanda mbuye wawo linalinso balalabalala pamalowo ndipo ena ankafufuza chakudya pamulu wazinyalalawo. Azibambo awiri anali ataima pachipata cholowera kumtayako ndipo zinkaoneka kuti akuuza anawo kuti akhale pamzere. “Kodi anawo akuima pamzere kuti atani?” anadzifunsa choncho. Chigalimoto chija chinalowa kumpanda kuja ndipo akhwangwala aja anayamba kuitsatira. Nawonso agalu aja ankathamangira cham’mbalimu, kuilondola kuyembekezera kuti atole phoso latsikulo. Chigalimotocho chitangokhuthula zinyalala zija, pamalo onsewo panangoti chifungo guu! Woyendetsa chigalimotocho anakhuthula zinyalalazo m’milu itatu. Atangomaliza, agalu, akhwangwala komanso ana aja anapita pamiluyo n’kuyamba kufukulafukula zinthu. Apa mpamene anamvetsa chimene chinkachitika. Zikuoneka kuti mwana aliyense ankayenera kupereka ndalama kuti alomwe kumtayako. Chimenechi chinali ngati chiphaso chomuloleza kulowa kumtayako kuti akakanganirane zinthu ndi agalu, akhwangwala, makoswe, ntchentche komanso tizilombo tosiyanasiyana todya zowola tomwe tinali pamalowo. Iwo ankasakasaka ulusi, zigamba, zikopa, zapapati za nsapato, malabala, zingwe, tomato owola, misonga ya mzimbe, makoko anthochi, mafupa ndi zina. 19