Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 199
Matigari
oweruza milandu, oyang'anira ndende ndiponso akuluakulu ena
a bomanu, ndikufuna kukuuzani kuti mwangotsala madzi
amodzi, masiku akucheperani! Ndibweranso mawa. Ife ndi an-
thu omenyera ufulu wadziko lathu omwe tinapulumuka: a
Matigari ma Njiruungi! Ndipo enanso ambirimbiri a ife tikubad-
wa tsiku ndi tsiku. John Boy, ndikufuna ndikuuze kuti
usadzagonenso m'nyumba yanga ija. Tiona kuti mwamuna ndi
ndani pakati pa iweyo ndi ineyo. Sindikunyengerera, ubweza
zanga zonse!"
Anthu onse anali m'chipinda muja anayamba kuwomba
m'manja.
Kwa kanthawi, apolisi anakhala ngati akuopa kupita
kukamugwira. Koma kenako anabwera n'kumumanga unyolo
ndipo anakamuponyera mumdima. Khamu la anthu anali
m'chipindacho linayamba kuwawooza apolisi aja. Kenako
anayamba kuimba kuti:
Ndionetseni munthu
Yemwe dzina lake ndi Matigari ma Njiruungi,
Yemwe akamayenda m’mapazi mwake m’malira maberu.
Komanso zipolopolo, ngindee!
Komanso zipolopolo, ngindee!
Nduna ija inayamba kuyankhula. Inayesetsa kuti mawu ake
amveke koma kuimbako kunangomiziratu mawu akewo. Ke-
nako anakuwa n'kunena kuti:
"Kodi si panja ndaletsa nyimbo zonse zokhudzana ndi
Matigari ma Njiruungi! Tsopano ndikuletsanso maloto onse! Li-
meneli ndi lamulo latsopano. Mwamva? Nyimbo zonse zaupan-
du komanso maloto onse ndi oletsedwa!"
198