Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 195
Matigari
a kusukuku yaukachenjede. Ndikufuna kuchenjeza ophunzira
amenewa kuti mkulu wa apolisi ali pomwe pano ndipo aka-
pitiriza kuyambitsa chisokonezo adziputira mavuto. Ngati
mukufuna kuimba, bwanji osamaimba nyimbo zovomerezeka
zomwe zili m'buku la So ngs o f a Parro t. Sindikufunanso kumva
nyimbo zina zoyambitsa chisokonezo. Zimene mwamva kwa
wophunzira uja ndi bodza lofuka utsi. Sukulu yaukachenjede
yatsekedwa chifukwa choti ophunzira anachita ziwonetsero
posagwirizana ndi chakudya chimene sukulu ikuwapatsa . . .
Ndi wophunzira m'modzi yekha amene watisiya atapondedwa
ndi anzake omwe amathawa . . . Koma sitinabwere pano kuti ti-
dzakambirane nkhani ya ophunzirayi . . . Ndiye bwanji ndipi-
tirize kuwerenga chigamulo chomwe oweruza athu odziwa
ntchitowa apereka. Ndikufuna kuti muiwaliretu nkhani imeneyi
msangamsanga, tamvana? Onse omwe anathawa kupolisi aja
akatsekeredwa kundende ndipo akaikidwa ku alimande mpaka
mlandu wawo utakaweruzidwa kubwalo lamilandu. Amenewa
anaweruzidwa kuti akatsekeredwe kundende yachitetezo
chokwima kwambiri mpaka nkhani yawoyi itaweruzidwa."
Kenako apolisi anawatenga n'kuyamba kutuluka nawo.
Munthu uja anamangidwa chifukwa chomangoyendayenda
m'tauni anakodola phwete la anthu atanena kuti popeza ali ndi
chitsimikizo choti kundendeko akapezako chakudya komanso
malo ogona, akuthokoza kwambiri oweruza aja chifukwa cho-
mukomera mtima mwanjira imeneyi.
"Tsopano tifike ku mlandu wa Ngaruro wa Kiriro. Oweruza
athu akhumudwa kwambiri ndi zimene munthu ameneyu
wachita. Kungochokera pamene tinalandira ufulu wathu
wodzilamulira, munthu wina sanayambepo watsutsa poyera
lamulo limene pulezidenti wapereka. Anthu ngati
194