Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 194
Matigari
Nthawi yomweyo wapolisi wina anagwira wophunzirayo
pakamwa. Atangomutseka pakamwapo, pakamwa pa mphunz-
itsi uja panatseguka. Mphunzitsiyo anapitiriza pamene
wophunzira uja analekeza:
"Tsopano ndazindikira kuti pali choonadi cha mitundu iwiri.
Choonadi china chimakhala cha anthu amene akuzunza
anzawo; pomwe china chimakhala cha amene akuzunzidwa! Ine
sindidzayerekeza kuimba ngati parro t, mpaka ndidzalowa
m'manda! Ine ndipitirizabe kuimba molimba mtima nyimbo ya
chiyembekezo yomwe ophunzira opanda mantha komanso an-
zeru aja amaimba."
Ndiyeno pamene ankati ayambe kuimba nyimboyo,
anangozindikiranso dzanja laphimba pakamwa pake. Tsopano
wophunzira komanso mphunzitsi uja anatengedwa n'kupititsid-
wa kwa asilikali oyang'anira ndende. Koma sanasiyebe kuchita
mavuvu. Chachitik achi si chilungamo ! Kenako kuchokera paka-
tikati pa anthu anali muholo muja, wina anakoleza moto
wanyimbo ija:
Ngakhale mutitsekere m'ndende,
Chipambano ndi chathu!
Chipambano ndi chathu!
Nyimboyo inakolera holo yonseyo ndipo onse anaimba ndi
mtima umodzi. Apolisi atazindikira kuti anthuwo afika posale-
letseka anayamba kuwomba mizinga. Ndiyeno pulofesa wokha-
zikika wa Parro to lo gy uja anayamba kunong'oneza Nduna
Yoona Zachilungamo ija. Posakhalitsa ndunayo inayankhula
mokuwa kwambiri kufika pamapeto pa mawu ake kuti:
"Chete! Aliyense akhale chete! Ndangotsinidwa khutu
posachedwapa kuti muholo ino mulinso ophunzira ena
193