Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 193

Matigari malamulo a m'dziko muno. Choncho ndine wokonzeka kugwiri- zana ndi chigamulo chimene oweruza athu apanga, chifukwa nanenso ndili pansi palamulo, ndipo ndimakhulupirira kuti oweruza milandu ayenera k uk hala m bali yoim a payo k ha. Chabwino, tsopano mvetserani chigamulo chimene chaperekedwa mosamala kwambiri." "Wophunzira komanso mphunzitsi ayenera kutsekeredwa m'ndende kuti aimbidwe mlandu wopezeka ndi zinthu zoletsed- wa. Makhoti sangalole kuti anthu ophunzira asokoneze anthu a m'dziko muno ndi ziphunzitso za Marx komanso ziphunzitso zi- na za chikomyunizimu." Wophunzira uja anamangidwa ndi unyolo limodzi ndi mphunzitsi uja. Zimenezi zinamuwawa mumtima koopsa ndipo analimba mtima ngati mkango n'kuyamba kuyankhula. Anali asanayambe wachitapo zangati zimenezi pamoyo wake. Anaku- wa kuti: "Muzikumbukira nthawi zonse zimene Matigari wakuuzani zija. Chiwanda chakuba sichikhutira ndi nsembe zimene anthu amachipatsa. Tsopano ndasukusula ndipo ndikutha kuona zime- nezi bwinobwino ngakhale m'chipinda muno. Ndipitirizabe kuimba mogwirizana ndi anzanga omwe anamangidwa dzulo komanso dzana, ndiponso ophunzira makumi asanu omwe aphedwa m'mawa walero ndi apolisi: Ngakhale mutitsekere m'ndende, Chipambano ndi chathu! Chipambano ndi chathu! Aliyense anangokhala chete. Tsopano anazindikira kuti mphekesera zoti ophunzira makumi asanu aphedwa zija ndi zo- ona. 192