Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 192
Matigari
Lemekeza atate wako ndi amako, monga Yehova Mulungu
wako anakulamulira; kuti masiku ako achuluke
Usaphe
Usachite chigololo
Usabe
Usamnamizire mnzako
Usasirire mkazi wake wa mnzako; usakhumbe nyumba yake
ya mnzako, munda wake, kapena wantchito wake
wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, ng’ombe yake,
kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako
Kenako anakhala pansi ndipo apa n’kutinso oweruza a
pompopompo aja akutuluka. Pambuyo pawo panali pulofesa
wokhazikika wa mbiri ya Parroto lo gy uja komanso wofufuza
milandu wovala chipewa choonetsa maso okha uja. Mtsogoleri
wa onsewa anali mzungu wina wachikulire, yemwe anapereka
chikalata chachigamulo kwa nduna ija.
Ndunayo inalamula kuti anthu onse omwe anagwidwa aja
apititsidwe kutsogolo kuti aliyense akamve chigamulo chomwe
alandire. Apolisi anapita kukawatulutsa m’chipinda chija ndipo
anawaika m’magulu atatu.
"Ndikufuna kuti nonsenu, kuphatikizapo alendo athu ole-
mekezeka omwe achokera ku USA, Britain, West Germany ko-
manso France, muone mmene timagwiritsira ntchito malamulo
m'dziko lachikhristu komanso lademokalase. Ndikudziwa
mayiko ena omwe anthu opalamula milandu ngati imene apal-
amula awayi amangonyongedwa kapena kuwomberedwa ndi
mfuti basi. Koma kuno timaonetsetsa kuti tikugwiritsa ntchito
malamulo moyenerera. Mwachitsanzo, ineyo ndine Nduna
Yoona Zachilungamo, komabe nanenso ndiyenera kumatsatira
191