Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 191

Matigari Ndalama zimene mukanamalandira zikanamakhala zokwanira kwa inuyo ndi azikazi anu. Koma pali njira inanso yabwino kwambiri yochepetsera chiwerengero cha anthu omwe ali m’dziko lino. Mimba ndi zotsatira za zilakolako komanso maganizo oipa. Ndikufuna ndipemphe boma kuti liletse kuti anthu asakhalenso ndi zilakolako komanso maganizo oipawa kwa zaka ziwiri. Tipempha apulezidenti kuti akhazikitse lamulo loti anthu osauka asiye kaye kukwatira kapena kukwatiwa chifukwa zimenenezi zikuchulutsa chiwerengero cha anthu m’dziko muno.” Anakwangula motero ndipo kenako anapita n’kukadzisomeka pampando anachoka paja. Ndiyeno Nduna Yoona Zachilungamo ija inayambanso kuyankhula. “Dera lino ndi lodala kwambiri pokhala ndi atsogoleri olingalira bwino ngati amenewa. Tsopano ndipemphe wansembe wathu kuti atiwerengere malamulo khumi. Ndikufuna nonse mutchere khutu kuti mumve malamulo a Mulungu.” Kenako anakhalanso pansi. Wansembe uja anatsegula Baibulo lake n’kuyamba kuwerenga. Anawerenga kuti: Usakhale nayo milungu ina koma ine ndekha Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe Samalira tsiku la Sabata likhale lopatulika, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira. Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito, ndi kuchita ntchito zako zonse; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usamagwira ntchito iliyonse 190