Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Página 189
Matigari
angatilembere mbiri yolondola yonena za dziko lathu
kuphatikizaponso mmene tinapezera ufulu wathu.”
“Nawonso mudzi womwe unapeka nyimboyi uyenera
kusinthidwa dzina. Ndi mudzi wamtundu wanji womwe
ungamadzitchule kuti Tram pville? Kodi kumudzi umenewo
kumangokhala anthu osowa pokhala komanso aumphawi? Kodi
akufuna kutiuza kuti alibe kulikonse kolowera? Ngati akufuna
thandizo angoyang’ana kuchipani cholamula, komanso kwa
mtsogoleri wa dziko lino Pulezidenti Ole. Ayenera kuchita
zimenezi mofanana ndi mmene anthu ena onse a m’dziko muno
akuchitira. Ndikufuna kulengeza pano kuti kuyambira lero,
dzina la mudziwu lasinthidwa. Tsopano lizidziwika kuti
Progressville. Ndiye tsopano anthu anga okondedwa aku Progressville,
iwalani za Matigari ma Njiruungi. Ame!”
Bwanankubwa uja anapita n’kukazidzalanso pamene
anafumuka, ndipo tcheyamani wachipani cholamula cha Kiama
Kiria Kirathana (KKK) anaimirira.* Tcheyamaniyu anavala
malaya ojambulidwa nkhope yapulezidenti komanso
chizindikiro chachipani, cha mbalame ya parro t. Pamunsi
pachizindikirochi panali zilembo za KKK. Zilembo zimenezi
zinalinso pakansalu kake kopukutira thukuta.
*Kiama Kiria Kirathana: (Gikuyu) kuimira ‘chipani cholamula.’
“Monga ine tcheyamani wachipani cha KKK kudera lino,
ndikufuna kuthokoza kwambiri kampani ya Aglo -american
popereka masheya kuchipani cha KKK. Tsopano fakitaleyi ndi
ya tonsefe. Tawaomberani m’manja eni kampaniyi azimayi ndi
abambo! Matigari ma Njiruungi akagwere uko! Tiyeninso
tisiyiretu kuimba nyimbo zotamanda munthu ameneyu
chifukwa zili ngati maloto oipa! Tsopano tiyeni tisamukire
kunkhani ya Karl Marx, nkhani ya ophunzira komanso ogwira
188