Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 188
Matigari
bata ndi mtendere wosaneneka. Sipakhalanso mikangano pakati
pa ogwira ntchito komanso owalemba ntchito . . . Koma pali
anthu ena omwe akumaimba nyimbo yomwe ingachititse kuti
ena asamamvere lamulo langokhazikitsidwa kumeneli lomwe
cholinga chake ndi kutilunzanitsa. Kambalame kena katiuza kuti
nyimbo imeneyi yapekedwa ndi anthu a m’mudzi wa
Trampville. Nyimboyo ikumanena kuti Matigari ma Njiruungi
akangoyendetsa miyendo yake, zipolopolo zikumalira kuti
ngindee. Tandiuzeni, mwamuona nokha munthu yemwe
akumamuti Matigariyo, yemwe anthu ambiri amamuimbira
nyimbo. Kodi zipolopolozo zili kuti? N’chifukwa chiyani
walephera kudzipulumutsa nazo? Matigari ma Njiruungi ali
m’tulo tatikulu, ndi wogona—ngati Rip Van Wink le . Rip Van
Winkle anali munthu wina wa ku Amerika yemwe anagona kwa
zaka zambirimbiri ndipo pamene ankadzuka, anapeza kuti
chilichonse chasintha. Zinthu zinali zitasintha kwambiri moti
ankangokhala ngati wadzuka kumanda ndipo anapeza kuti
zinthu sizikuchitikanso ngati mmene zinkachitikira asanagone
tulo taketo.”
“Tsopano mundimvetsere mosamalitsa. Kuyambira lero
nyimbo imeneyi ndisadzaimvenso. Ndisadzamvenso wina
akuimba, kukamba kapena kutchula za Matigari ma Njiruungi.
Munthu amene adzapezeke akuchita zimenezi adzaona
polekera. Nkhani zimene tikufunika kumakambirana ndi
zokhudzana ndi chituk uk o basi. Sitikufuna kumakambirana
zinthu zankutu ngati za Matigari ma Njiruungi. Ndikufuna kuti
aliyense aiwaliretu za nkhani ya Matigari ma Njiruungi. Tsopano
tiyeni timvane chimodzi ngati mmene zimachitira mbalame za
parrot n’kuvomereza kuti nkhani ya Matigari ma Njiruungi
inangokhala ngati maloto oipa. Tili ndi mapulofesa omwe
187