Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 187
Matigari
ndi kadaulo pankhani yonena zoona zenizeni zosawonjezera
thendo. Mkulu mukumuona apayu azimufunsa ngati munthu
amene wapalamula mlandu akunena zoona kapena zabodza.
Akapukusa kapena kugwedeza mutu, azidziwa zimene
akutanthauza. Kodi mukudzidwa chifukwa chake nthawi zonse
amanena zoona? Chifukwa amachita akafukufuku pa nkhani
zambirimbiri zimene zikuchitika, amafufuza paliponse . . .
Ndinakuuzanitu ine! Maso komanso makutu aboma lathu ali
ponseponse. Chabwino, tsopano tiyeni tidikire chigamulo . . . "
Pulofesa wokhazikika wa mbiri ya Parro to logy, mkonzi wa
nyuzipepala ya Daily Parro to lo gy, mphunzitsi wa Ph.D ya
Parrotology komanso wofufuza milandu wovala chipewa choonetsa
maso okha uja anadzuka n’kupita kuchipinda anatsekera
Matigari, Ngaruro wa Kiriro komanso anthu ena aja.
“Pamene akuluakuluwa akumvetsera milandu imene
anthuwa apalamula, ndipemphe bwanamkubwa watauni ino
komanso tcheyamani wachipani wadera lino kuti atiyankhule
mawu awiri atatu.”
Bwanamkubwa watauniyo anaimirira. Iye anavala buluku
ndi jekete yakhaki. Anavalanso chipewa komanso mandala
aakulu zedi. Komanso anavala taye yolembedwa KKK. Buluku
komanso jekete anabophayo inali yokhuthala kwambiri moti
inkaoneka kuti ikumulemera. Kenako anatsokomola
modzitukumula kwambiri asanayambe kupukusika:
“Ndilije zambiri zoti ndinene. Anduna athu anena kale
zambiri zomwe zimafunika kunenedwa. Zimene anduna athu
amachita zimakhala zachilungamo komanso zolondola. Mfundo
zina zimene anena tsopano ndi malamulo omwe tikufunika
kumayendera. Tikachita zimenezi m’dziko muno mukhala
186