Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 186
Matigari
Chifukwa choti zimenezi ndi zizindikiro za maudindo awiri
akuluakulu amene ndanyamula. Udindo woyamba ndi
kuwonetsetsa kuti malamulo a m’dziko muno akutsatiridwa,
ndipo udindo wachiwiri ndi kuwonetsetsa kuti m’dziko muno
muli choonadi ndi chilungamo. Kodi munaona mmene mkulu
wapolisi uja anatulutsira mfuti yake? Tsopano yafika nthawi yoti
ndikuuzeni za anthu ena omwe akuonetsetsa kuti m’dziko
muno muli choonadi ndi chilungamo. Mwawaona akuluakulu
avala mikanjowo? Amenewo ndi oweruza komanso maloya.”
“Ineyo ndimagwirizana kwambiri ndi mawu achingerezi
akuti, justice d elayed is justice d enied .* Sikuti tiyenera
kungoonetsetsa kuti chilungamo chikuchitika, koma anthu ena
ayenera kuona ndi maso awo kuti chikuchitikadi. Choncho
ndikufuna muone ndi maso anu chilungamo chikuchitika.
Ndikuganiza kuti ndine nduna yokhayo padziko lonse imene
imayenda ndi anthu oweruza milandu n’cholinga choonetsetsa
kuti chilungamo chikuchitika pompopompo. Akuluakulu
amenewa akalowa m’chipinda mwatsekeredwa anthu
apalamula milandu aja kuti akamve milandu yawo. Chigamulo
chiperekedwa pompano msonkhanowu usanafike kumapeto.”
*Mawu achingereziwa angatanthauze: Kuchedwetsa chilungam o n’chimodzimodzi
kukaniza kuti chilungamo chichitike.
"Akuluakulu amenewa athandizidwa ndi pulofesa
wokhazikika wa mbiri ya Parroto lo gy, mkonzi wa nyuzipepala
ya Daily Parro to lo gy, mphunzitsi wa Ph.D ya Parro to lo gy
komanso wofufuza milandu wovala chipewa choonetsa maso
okha uja. Kodi munthu wovala chipewayu mukumudziwa?
Ndikunena uyu wavala chipewa choyerayu? Ndikudziwa kuti
ambiri a inu munkadana naye kwambiri m’thawi ya atsamunda.
Koma wapanoyu ndi wabwino chifukwa zimene amanena ndi
choonadi ndi chilungamo. Iyeyu ali ngati mboni yaboma yemwe
185