Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 185

Matigari wabwera pagulu ngati pano n’kumadzitukumula kuti ali ndi chikalata cha nyumba. Chikalata chake chiti? Akuti magazi komanso thukuta lake! Ndani angamve zakuntchini kwadzadza ngati zimenezo! Ndi ndani amene angakhulupirire munthu atamanena kuti ali ndi nyumba koma alibe mapepala osonyezadi kuti nyumbayo ndi yake? Munthuyu wapalamulanso mlandu woima pachulu n’kumadzitama kuti anapha anthu!” "Kodi dzikoli likanakhala lotani zikanakhala kuti anthu okhawo amene amalima ndi amene amaloledwa kudya? Kodi dzikoli likanakhala bwanji zikanakhala kuti ogwira ntchito akakhala kuti sakugwirizana ndi zimene owalemba ntchito akuchita amangotenga zida n'kuyamba kumenyana nawo m'malo mothetsa nkhani mwamtendere komanso mwachilungamo ngati mmene ndachitira ine lero? Bwenzi pali chisokonezo chokhachokhatu padzikoli. Ndithu bwenzi pali chipwirikiti chenicheni! Muzikumbukira kuti, kuti dziko lililonse liyende bwino pamayenera kukhala magulu atatu awa: olemera monga anthu a mabizinezi komanso amakampaniwa; asilikali ndi apolisi, monga awa akukhazikitsa chitetezowa (nonse munaonanso mmene mkulu wa apolisi anatulutsira mfuti yake mwaluso); ndipo gulu lachitatu ndi atsogoleri monga ine ndili pano, kapena ansembe, komanso ena omwe nditakuuzeni posachedwapa. Ndiye taona kuti olemera, asilikali komanso atsogoleri ndi anthu omwe amafunikira m’dziko kuti zinthu ziziyenda bwino." “Ndikufuna ndikusonyezeni mmene utsogoleri weniweni uyenera kukhalira. Ndikufuna nonse mudziwe kuti ine ndine nduna ya zachilungamo. Mwaiona suti ndavalayi? Mukhoza kuona kuti m’katimunso muli kajekete kena, azungu amati kawisikoti. N’chifukwa chiyani ndavala zinthu ziwiri? 184