Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 184
Matigari
Apolisiwo anapeza kuti Matigari analibe chida chilichonse,
ngakhale mpeni. Komabe, ngakhale sanapeze chida,
anamukwidzingabe ndi unyolo. Ankaona kuti si bwino
kupereka mpata kwa Dyabolosi ngati ameneyu, yemwe zolinga
zake sizinkadziwika bwinobwino.
Zitangotero, alendo onse omwe anali kutsogolo kwa holoyo,
anatulutsira limodzi tinsalu tawo topukutira thukuta ngati
anachita kupangana. Kenako anayamba kupukuta zipumi zawo
zomwe zinali zitanona bwino ndi thukuta. Iwo anaupezano
mtima atazindikira kuti Matigari analibe mfuti. Apolisi aja
anatenga Matigari n’kukamutsekera kuchipinda kunali Ngaruro
wa Kiriro komanso anthu ena aja. Munthu yekhayo amene
panalibe pagululi, yemwe anathawa kundende kuja, anali
Giceru yekha basi.
Kenako mkulu wa apolisi uja anabwezera mfuti yake ija
m’chimake akuoneka kuti akuchita manyazi kwambiri
posonyeza mantha aakulu pamaso pa gulu la anthu.
Nduna ija inkaoneka kuti yasokonezeka. Inkakhala ngati
ikusakasaka ulusi wa nkhani imene ingatole kuti ipitirize
msonkhanowo. Kenako inatsokomola mochotsa akalungusese
kukhosi. Kenako inanena kuti:
“Anthu amene amakonda kuimba mlandu boma lathu
adzionera okha zimene zachitikazi! Kodi akuganiza kuti boma
lingamasekelele anthu ngati amenewa? Nonse mwamva zimene
munthu uja wanena! Ndisakunamizeni, munthu uyuyu ndiye
wapalamula mulu wamilandu. Ali ndi mlandu wopezeka
pamalo a eni popanda chilolezo. Anathawa kupolisi. Wakhala
akumangozungulira paliponse n’kumauza anthu kuti iyeyo ndi
Matigari, zomwe ndi bodza lenileni. Kuwonjezera pamenepo,
183