Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 182
Matigari
Mtsamunda Williams nayenso ndi uyo, komanso mkulu wa
apolisi ndi uyo waima apoyo. Afunseni ngati zimene
ndikunenazi zili zabodza. Chomwe ndikupempha m’dziko
lademokalaseli ndi choonadi komanso chilungamo, zimenezo
ndi zimene ndikufuna. Ndikufuna kuti chilungamo chioneke.”
Pa nthawiyi n’kuti Robert Williams ndi John Boy
akunong’onezanabe. Kenako Boy analemba kapepala
n’kumupatsira mkulu wa apolisi uja.
“Kodi inuyo ndi ndani bambo?” inafunsa nduna ija.
“Matigari ma Njiruungi,” anayankha motero.
Nduna ija inachita mantha. Kenako inatulutsa kansalu
kopukutira thukuta kuchokera m’thumba mwake ndipo
inayamba kupukuta khope yake yomwe inali thukuta
lokhalokha. Ndiyeno mkulu wa apolisi uja anayankhula
monong’ona kwa ndunayo. Onsewa ankaganizabe kuti Matigari
ali ndi mfuti m’thumba mwake. Ankadzifunsa kuti, ‘Nanga
n’chifukwa chiyani sakutulutsa manja m’thumbamo?’ Ankaona
kuti kalipokalipo. Komanso ankadabwa kuti, ‘N’chifukwa
chiyani akuyankhula molimba mtima choncho?’ Ankaona kuti
ayenera waponda mwala. Koma pa nthawiyi sakanaombera
Matigari popanda kuika moyo wa anthu ena omwe anali
muholoyo pangozi, makamaka alendo ofunikira kwambiri
omwe anakhala kutsogolo kwa holoyo. Choncho anadikira kaye.
Tsopano Matigari anali ataima chapakatikati pa holoyo. Ndipo
anthu onse anangokhala duu akumuyang’ana momusirira.
Panali patadutsa zilumika zambiri kuchokera pamene anaona
munthu wolimba mtima choncho! Iwo anayamba kuona kuti
n’zoonadi kuti anthu omwe ankamenyera ufulu wadziko anali
adakalipo. Iwo ankadziuza kuti, ‘Zoonadi eti anthu omenyera
181