Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 181
Matigari
“Nkhani yanga si yaitali,” Matigari anatero, “Komanso sikuti
ndi yaifupi. Ndi nkhani imene nonse mukuiona m’holo ino.
Nkhani yanga yapangidwa ndi inuyo komanso ineyo. Ine
ndinamanga nyumba. Ndinalima munda. Ndinagwira ntchito
mwakhama kufakitale. Koma Mtsamunda Williams
mothandizidwa ndi wantchito wake, John Boy, anatenga zonse
n’kulemera nazo. Ndinkadziuza kuti: ‘Mavuto amene
angakhalepo pakati pa wakuba ndi woberedwa ayenera
kuthetsedwa ndi nkhondo basi.’ Choncho tinayamba
kulimbanapo. Williams ndi John Boy anali mbali imodzi, ndipo
ine ndinali mbali inayo. Kwa zilumika zambiri tinakhala
tikusakanasakana. Tinkasakana kuti tione amene atayambirire
kugwetsa mnzake. Choyamba ndinagwetsa John Boy.
Mtsamundayo sakanachita kanthu popanda kuthandizidwa ndi
wantchito wakeyu. Mtsamunda Williams sakanagwedeza
maziko a nyumba yanga popanda womuthandiza. Kenako
pamapeto pake nayenso ndinamugwetsera m’dothi.
Ndinayamba ndi kukantha Boy, ndipo kenako ndinalikha
Mtsamunda Williams. Dzulo ndabwerera kwathu kuno
kuchokera kunkhalango. Ndinali ndi chisangalalo chodzadza
tsaya, ndipo m’thupi mwangamu ndimamva kukoma koopsa
podziwa kuti ndagonjetsa adani anga. Koma mukudziwa amene
ndamupeza ataima pageti la nyumba yanga? Mwana wa Boy, ali
limodzi ndi mwana wa Mtsamunda Williams. Iwo anandifunsa
kuti: ‘Kodi chikalata chosonyeza kuti nyumbayi ndi yako chili
kuti?’ Ndipo ine ndinawafunsa kuti: ‘Kodi mukufuna chikalata
chinanso chamtundu wanji kuposa thukuta komanso magazi
omwe ndinakhetsa pomanga nyumbayi?’ Iwo anakana
kundipatsa makiyi a nyumba yanga, ndipo anaitana apolisi kuti
andimange. Apolisiwo ananditenga n’kukanditsekera kundende.
Mwana wa Boy ndi uyo ali apoyo, ndipo mwana wa
180