Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 180
Matigari
ukaifunse funso limeneli ndipo ine ndinamumvera. Ndiye funso
langa nali: Womanga anamanga nyumba. Munthu wina yemwe
ankangoonerera nyumbayo ikumangidwa anabwera
n’kulowamo. Womanga uja anayamba kugona panja, pamtetete
popanda ndi denga lomwe.
Telala anasoka zovala. Munthu wina yemwe sadziwa
n’komwe kuti ulusi timalowetsa bwanji pasingano, anabwera
n’kuyamba kuvala zovala zija. Telala uja anayamba kuvala
zigamba n’kumavutika ndi usiwa.
Wolima anasamalira munda wake. Munthu wina yemwe
amangokolola pamene sanafese anatenga zokololazo. Iye
ankayasamula chifukwa cha kukhuta, pomwe wolima uja
ankayasamula chifukwa cha njala.
Wogwira ntchito anapanga zinthu zosiyanasiyana. Anthu
ochokera kunja komanso nthata zoyamwa anzawo magazi
zinatenga zinthuzo n’kuzigulitsa. Wogwira ntchito uja anatsala
manja ali m’khosi, popanda olo ndi wamtambala yomwe.
Ndiye funso langa ndi lakuti, kodi choonadi ndi chilungamo
chabisala kuti m’dziko muno?”
Nduna yoona zachilungamo ija inaima kaye pang’ono
mosonyeza kuti ikudya mutu n’cholinga choti ipeze kaye
chonena isanayambe kuyankha funsolo.
“Siyani kuyankhula m’mafanizo. Ngati mukufuna kufunsa
funso, ingofunsani funsolo mwachindunji, m’chichewa
chosavuta. Musaope chilichonse. Fotokozani momasuka mavuto
anu onse ndipo ine ndikuthandizani. Munthu wamulunguyo
anachita bwino kwambiri kukutumizani kwa ine, sanalakwitse
ngakhale pang’ono. Mwabwera kwa munthu woyenerera.”
179