Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 18

Matigari Gawo 5 Pachipata cha fakitaleyo panali chikwangwani cholembedwa ndi mawu akuluakulu kuti: ANGLO-AMERICAN LEATHER AND PLASTIC WORKS MALOWA NDI A ENI Palibe Njira Fakitaleyo inali yaikulu kwambiri ndipo inazunguliridwa ndi mpanda wawaya. Fakitaleyo inali mkati mwa mpanda wamalata ndipo mpanda wakunja unali wawaya wamingaminga. Kenako anaona chigalimoto chofiira chikutuluka m’fakitaleyo. Chinali ndi ngolo zitatu zodzadza ndi zinyalala. Mlonda anapita kutsogolo kwa chigalimotocho n’kukakweza chitsulo chomwe chinatchinga pachipatapo ndipo chigalimotocho chinatuluka. Chitatuluka chinayamba kulowera kumene kunali chikwangwani china chokembedwa kuti, “MSIKA WAMASAMBA.” Kenako anayamba kupita kuchipata kuja. Mlonda uja anali atakhala pampando. Anavala yunifomu yakhaki komanso chipewa chofiira chokhala ndi ziyaliyali. Pajekete yake panalembedwa kuti, “Katundu wa Kampani Yaulonda.” Pafupi ndi miyendo yake panali kambaula kamakala kopangidwa ndi chitini. Bambo uja anadzifunsa kuti, “N’chifukwa chiyani munthu ameneyu akuotha moto kutentha kumeneku? Mwinatu malungo amupezeketsa?” Kenako anazindikira kuti mlondayo ankaotcha gunya. Bamboyo anaona kuti angachite bwino kufunsa mlondayo kuti amuthandize kupeza abale ake mufakitaleyo. Popeza pafakitaleyi panali khwimbi la anthu, sankakayikira kuti akhoza kupezapo m’bale wake. Ankaganizanso kuti mwina mlondayo akhoza kudziwa 17