Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 179

Matigari wa anthu monga Russia ndi China.” Matigari anayenda molowera chapakati paholoyo ndipo m’mbali mwake munali anthu ali ndindindi. Pamene ankapitiriza kuyankhula, manja ake adakali m’matumba achijasi chake chija, palibe amene anayerekeza kutsokomola, kudzikanda kapena kupanga phokoso lililonse ngakhale laling’ono kwambiri. “Mwafunsa kuti, n’chifukwa chiyani anthu sakufunsa mafunso? Ndikuyankhani funso limeneli. Kuchita zinthu mosamala sikutanthauza kuti munthu ndi wamantha. Nthawi ina Kambuku anafunsa Kalulu kuti: ‘Bwanawe, n’chifukwa chiyani sunayambe wabwerapo kunyumba kwanga kudzacheza?’ Kalulu anayankha kuti: ‘Ndakhala ndikuonapo anthu ambirimbiri akulowa m’nyumba yakoyi, koma sindinayambe ndaonapo ngakhale m’modzi akutuluka.’ Anthu onse mukuwaona apawa ali ngati Kalulu ameneyu. Ali ndi makutu komanso maso, omwe amawagwiritsa ntchito kuona komanso kumva zimene zikuchitika pamalo amene ali. Koma ndikufuna kuuzabe anthu amenewa kuti: Mantha akachuluka m’dziko mumachitika zoipa zambiri. Ndiye ngakhale ndikudziwa bwinobwino zimene Kalulu anauza Kambuku, ndichitabe zaukadziwotche pokufunsani funso inu a Nduna Yoona Zachilungamo. Ine ndakhala ndikuzungulira kwa tsiku lonse kufufuza munthu woti ayankhe funso langa. Ndayenda ngodya zonse zadzikoli pa m atatu komanso pa mitundu yonse ya galimoto. Ndayankhula ndi asing’anga, ophunzira, aphunzitsi komanso anthu openda nyenyezi zamakono. Munthu wina wanzeru, yemwe amawerenga mawu a Mulungu anandiuza kuti: ‘Pita kwa Nduna Yoona Zachilungamo 178