Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 178
Matigari
ataona zimene zinachitikira Ngaruro wa Kiriro. Kuwonjezera pa
kuona zimene zinachitikira Ngaruro, aliyense muholoyo anali
atazunguliridwa ndi apolisi.
Matigari ndi nduna yoona zachilungamo ija anaima
moyang’anizana.
Apolisi awiri anayamba kuchita zinthu ngati akufuna
kumugwira. Koma Matigari anangoti maso ga pa nduna ija
ndipo anayamba kuyankhula mokweza kwambiri moti aliyense
m’chipindacho ankatha kumumva bwinobwino. Ndi mawu
amphamvu ngati chitsulo, anachenjeza apolisi ankafuna
kumugwira aja. Iye anati: “Tangoyerekezani kutambasura dzanja
lanu n’kundigwira muone! Nanenso ndine wakale kwambiri
mofanana ndi dziko lathuli.” Mawu a Matigari sankasonyeza
dontho la mantha ngakhale limodzi. Kulimba mtima komanso
mphamvu za mawu ake zinachititsa kuti apolisi awiri aja achite
mantha n’kubwerera m’mbuyo. John Boy Junior ndi Robert
Williams anayamba kunong’onezana, koma sanasiye kuyang’ana
Matigari. Mkulu wa apolisi uja anapita n’kukanong’oneza nduna
ija ndipo anachita zimenezi chidwi chake chili pamanja a
Matigari omwe anali adakali m’thumba mwa chijasi chija.
“N’kutheka kuti ali ndi mfuti. Ndiye ingomulolani kuti
apitirize kuyankhula, kwinaku ife tikusakasaka njira yoti
timuwomberere.”
Nduna ija inayamba kukhala ngati yayamba kufufuza lilime
lake lomwe linasokonekera. Italipeza inanena kuti, “Musiyeni
ayankhule!” Inayankhula zimenezi mokweza kwambiri kuposa
mmene zinafunikira. “Pajatu ndanena kuti aliyense amene ali
ndi funso akhoza kufunsa! Boma lathuli limalemekeza ufulu
wachibadwidwe. Silili ngati mayiko ena omwe salemekeza ufulu
177