Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 177

Matigari ena n’kukamutsekera kundende. Palibe boma limene linganyengerere munthu wovutitsa komanso kulola kuti munthu m’modzi aphwanye maufulu a anthu mamiliyoni ambirimbiri omwe ali m’dziko muno. Ndi ndani amene angalolere kutaya thumba lathunthu lachimanga chifukwa choti chimanga chimodzi n’chowola? Amangochotsa kachimanga kowolako n’kukataya. Eetu! Nacho nso chim anga cho tsalacho chili ndi ufulu wawo!” “Ndiye musatichititse manyazi pamaso pa alendowa. Tamafunsani mafunso. Sitikufuna kuti wina akawotche gombeza! Ndikubwerezanso, pali wina amene ali ndi funso?” “Inde!” Munthu wina anatero. Maso a anthu onse anali m’chipindacho anatembenukira kwa munthuyo yemwe anali chakukhomo kwenikweni kwa holoyo. Munthu wamtali, wathupi lodzinga komanso wooneka wachikulire, anaima chapakhomo. Pamutu pake panali chipewa chakhonde, chomwe anachimanga ndi chingwe pachigama pake. Chipewacho chinali chokongoletsedwa mikanda ndipo chakutsogolo kwake kunazikidwa nthenga yanthiwatiwa. Anavala chijasi cholekeza m’mawondo ndipo chijasicho chinali chopangidwa ndi chikopa chakambuku. Anali atavala buluku lansalu yokhuthala kwambiri yoti kuimika pansi ikanatha kuima yokha. Manja ake anali atawalowetsa m’matumba a chijasicho mokhala ngati wagwira chinachake. Guthera komanso Muriuki omwe analinso m’holoyo anayang’anizana modabwa. Aliyense anangokhala chete ali dwii kuti aone zomwe zitachitike. Iwo sankakhulupirira kuti munthu wanzeru zake angachite za ukadziwotche ngati zimenezo n’kufunsa funso 176