Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 176
Matigari
ntchito yanu! Mwina nayenso ndi mmodzi mwa anthu amene
akuphunzitsa chiphunzitso cha Karl Marx m’dziko muno.”
Apolisi awiri anagwira Ngaruro wa Kiriro ndipo
anakamuponyera m’chipinda munali anthu ena anagwidwa aja.
Zimenezi zinachititsa kuti anthu aluse n’kuyamba kukuwa
mokalipa. Nthawi yomweyo mkulu wa apolisi uja anaimba
wizilo yake. Apolisi anali panja aja komanso anali m’mawindo
aja analowa muholoyo. Zimenezi zinachititsa kuti anthuwo
akhale pakati pa apolisiwo ndipo analibe kothawira.
“Pali winanso amene ali ndi funso?”
Atangonena zimenezi, m’holoyo munangoti zii. Kenako
anapitiriza kuyankhula ngati kuti palibe chilichonse chodetsa
nkhawa chimene chachitika.
“Mwina ndibwerezenso. Pali winanso amene ali ndi funso
ngati?”
Palibe amene anayankhula onse anangoti chete. Nduna
Yoona Zachilungamo ija inapitiriza kunena kuti: “N’chifukwa
chiyani simukufuna kufunsa mafunso? Nokhanso mukudziwa
kuti tili ndi alendo ochokera kumayiko a azungu pano, a ku
USA, Britain, West Germany komanso France. Alendo
olemekezeka amenewa akuchita kafukufuku. Akufuna kudziwa
mmene boma komanso chipani cha dziko lino chikuyendetsera
zinthu. Akufufuzanso mmene mabungwe ena omwe si aboma
akugwirira ntchito zawo m’dziko muno. Ndikufuna adziwonere
okha mmene chik o m yunizim u cha kuno ku Africa
chimayendera. Dziko lathu lino ndi lademokalase ndipo
timaonetsetsa kuti malamulo akutsatiridwa. Choncho boma lili
ndi mphamvu zochotsa munthu amene akusokoneza
175