Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 175
Matigari
lamulo limene laperekedwa; chachiwiri, waphwanya malamulo
awiri amene mtsogoleri wadziko lino wapereka. Waphwanya
lamulo lomwe ndangolilengeza mphindi zingapo zapitazo,
ndipo aliyense anamva ndikunena zimenezi. Ndinanena kuti
kuyambira lero kuchita sitiraka ndi koletsedwa, ndikunama
kapena? Ndinanenanso kuti m’dziko muno musadzapezekenso
munthu wochita kapena kulimbikitsa anzake kuti achite sitiraka.
Munthuyutu akulimbikitsa ena kuti apitirizebe kuchita sitiraka.
Kuchita zimenezi ndi mwano waukulu chifukwa ndiye kuti
akukana kutsatira zimene mtsogoleri wa dziko lino walamula.
Kodi mukudziwa lamulo limene waphwanya polimbikitsa ena
kuti asamvere zimene pulezidenti wathu walamula?
Akuphwanya lamulo la sed ictio n komanso treaso n, lamulo
lolimbikitsa ena kugalukira komanso kuchitira chiwembu
pulezidenti. Mwina nanenso n’tafunsa: Kodi makampani
angayende bwanji ngati ogwira ntchito atamasankha okha
mabwana oti awalembe ntchito komanso malipiro amene
akuyenera kulandira? Nanga zinthu zingakhale bwanji ogwira
ntchito atamasankha okha nthawi imene akufuna kupuma
komanso imene akufuna kugwira ntchito? Ngati anthu akufuna
zimenezi, bwanji osangotsegula makampani awo? Bwanji
osangodzilemba ntchito okha m’malo momayenda mimba
tiyetiye m’mafamu komanso makampani a eni n’kumakafunsira
ntchito? Kumenekutu ndi kuzerezeka kwakukulu! Munthu
amene wayankhula uja wakana kugwira ntchito ndipo aliyense
wadzimvera mumtolo munthuyu akutafula zimenezi. Ndi ufulu
wake kukhala osamagwira ntchito, palibe angamuletse. Koma
alibe ufulu wolimbikitsa ena kuti nawonso atengere maganizo
ake oipawa. Kodi mungamuthandize bwanji munthu yemwe
wasankha kumangokhala? Anthu aulesi ndi amene amakonda
kudandaula komanso kuyambitsa mavuto. Apolisi! Gwirani
174