Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 174
Matigari
wa malonda amene tikugulitsa ndipo tichita zimenezi mpaka
ogulawo atavomereza pempho lathu. Chomwe tikupempha ndi
choti atiwonjezere malipiro kuti tizikwanitsa kupeza zofunika
pamoyo, malinga ndi mmene mitengo ya zinthu yapengeramu.
Zinthutu zikukwera mtengo tsiku ndi tsiku! Tikhala bwanji ndi
moyo ngati tikupatsidwabe ndalama yomwe tinagwirizana zaka
20 zapitazo, zinthu zikadatchipa! Ndalamatu zimene
tikupatsidwa panopa ndi zofanana ndi zomwe ena akumapatsa
ana awo kuti akadyere kusukulu! Choncho tingakonde kuti
malipiro azikwera mogwirizana ndi mmene ndalama yathu
ikuyendera, ikagwa pansi malipironso azikwera.
Tikupemphanso kuti tizipuma Loweruka, apo ayi tizilipidwa
ndalama yoonjezera monga o vertim e. Nafenso timakhala ndi
zochita zathu kumapeto kwa mlungu moti sitingalole
kumangogwira ntchito yapwitika. Ngati akufuna tizigwira
ntchito, azitilipira. Tikupemphanso kuti John Boy komanso
Robert Williams achotsedwe m’gulu la anthu oyendetsa
kampaniyi ndipo pasankhidwe anthu ena kuti alomwe m’malo
mwawo. Anthu awiri amenewa ndi ankhanza komanso ouma
mitima ngati mfiti zazikazi. Anthu amenewa anyanya moti
amaposanso anthu omwe ankatilamulira m’nthawi ya
atsamunda."
Atangomaliza kunena zimenezi, Ngaruro wa Kiriro anakhala
pansi. Ogwira ntchito onse anawomba m’manja osati pang’ono,
azibambo anaimba malikweru ndipo azimayi anabulumunya
nthungululu.
Nduna ija inadikira kaye kuti kuwomba m’manjako kuzizire.
Kenako inati: “Mwamva nokhatu mwano umene munthuyu
wageya, si choncho? Munthu ameneyu wachita zinthu
zophwanya malamulo maulendo atatu. Choyamba, sanamvere
173