Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 173
Matigari
Ngaruro wa Kiriro anaimirira:
"Ndaima kuti ndiyankhule m'malo mwa ogwira ntchito
anzanga. Ndikufuna kukuuzani kuti mkangano komanso
mavuto amene tikunenawa ali pakati pa mbali ziwiri: oyendetsa
kampaniyi komanso ogwira ntchito, osati ndi boma kapena
chipani ayi. Pamene pakhota mchira wanyani ndi poti ogwira
ntchitofe tikuponderezedwa koopsa. Timagwira ntchito
yolemetsa kwa maola ambirimbiri, koma timalandira malipiro
ochepa zedi. Ifeyo tikuipangira kampaniyi phindu losaneneka,
mamiliyoni ambirimbiri. Koma omwe anatilemba ntchitowa
ayenera kuzindikira kuti amapeza mpindu lonselo chifukwa
chakhama lathu. Chigamulo chimene mwapereka pankhaniyi si
chachilungamo komanso ndi chokondera. Chikungosonyezeratu
kuti inuyo, a m’boma komanso chipani cholamula, muli
kumbali ya kampaniyi komanso anthu ena omwe ali ndi
mafamu akuluakulu m’dziko muno. Koma ndili ndi funso
limodzi: Kodi boma lathu, boma la ogwira ntchito lili kuti? Ifetu
sitikupemphetsa zinthu zaweni, tikungofuna tipatsidwe zinthu
zathu basi. Tizilipidwa malipiro ogwirizana ndi ntchito imene
timagwira. Kuti ifeyo tikhale ndi moyo zimadalira ntchito imene
timagwirayi. Khama lathu ndi limene lili katundu yekhayo
amene tili naye pamoyo wathu. Ife timagulitsa khama lathulo
m'misika. Tandiuzeni inu omwe mumadziwa zamalonda: Ngati
munthu wogula sakufuna kupereka ndalama za chinthu
chimene akufuna, kodi si paja wogulitsayo amakhala ndi ufulu
womukaniza chinthucho mpaka atapereka ndalama imene
wauzidwa? Ndipo mungandivomereze kuti nthawi zina
amakambirana, mwinanso kuchotserana n’kugwirizana mtengo
umene wogulayo angakwanitse. Masitiraka amene tikuchitawa
akufanana ndi zimenezi. Tikukana kugwira ntchito chifukwa
ndalama imene tikupatsidwa sikugwirizana ndi mtengo
172