Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 172
Matigari
“Tsopano mvetserani chigamulo chomwe ndikufuna kupere-
ka chokhudza oyendetsa kampani komanso ogwira ntchito.
Choyamba, ndikulamula ogwira ntchito onse kuti abwerere
kuntchito zawo kuyambira lero ndipo asadzayerekezenso ku-
chita sitiraka. Zamveka? Kungoyambira panopa, masitiraka
asadzachitikenso m’dziko muno. Ndipo ndikupempha oy-
endetsa kampaniyi kuti alembenso ntchito aliyense amene
amagwira ntchito pakampaniyi, kupatulapo amene
amatsogolera komanso kumapandutsa anzawo kuti achite
sitiraka. N’chifukwa chiyani ndapempha kampaniyi kuti ichite
zimenezi? Chifukwatu kampaniyi inali itakonza kale zochotsa
ntchito anthu onse omwe anachita sitiraka. Imafuna kuti ilembe
ntchito anthu ena atsopano. Ndipo ndikuuzeni, mwina
simukudziwa. Anzanu akumaswera tsiku lonse kufufuza ntchi-
to m’taunimu! Ndiye osaseweretsa mwayi umene muli na-
wowo! Ndikuganiza kuti ndapereka chigamulo chabwino ko-
manso chosakondera pankhaniyi. Ndi ndani akung’ung’udza-
yo?”
“Ndisanamalize, ndikufuna kudziwitsa aliyense m’dziko
muno kuti masitiraka aletsedwa ndi mtsogoleri wadziko lino.
Kale tikulamulidwa ndi atsamunda tinkapanga masitiraka
chifukwa tinkafuna ufulu wathu. Ndiye panopa sitingamapan-
genso masitiraka chifukwa ufulu tili nawo kale. Ili ndi boma
lathu, boma la ogwira ntchito! Kuwonjezera pamenepo, mtsogo-
leri wa dziko lino, Pulezidenti Ole, nayenso ndi wogwira ntchi-
to. Ndi wogwira ntchito nambala wani. Choncho boma lathuli
likulamulidwa ndi wogwira ntchito mnzathu yemwe amadziwa
bwino mavuto athu. Sindikuganiza kuti pangapezekenso mfiti
ina yomwe singayamikire mwayi umenewu! Ine ndiimire pame-
nepa, pali funso ngati?”
171