Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 171

Matigari “Anthu amenewa asenza maganizo awo oukirawo n’kupita nawo ku Soviet Union, China, North Korea, Cuba kapena Alba- nia. M’dziko muno sitikufuna anthu otikokera m’mbuyo ayi! Bwanji osamaphunzira komanso kuphunzitsa mtundu wa chikomyunizimu womwe kampani ya Leather and Plastics yati- sonyeza pano? N’chifukwa chiyani mwangokhala duu osaomba m’manja? Aa, akuluakuku tachitani manyazi! N’chifukwa chi- yani nanunso azimayi simukululutira posangalala ndi zimene kampaniyi yachita? Ayi, paja nthawi zina pamatenga nthawi kuti munthu azindikire madalitso aakulu amene amugwera. Chifukwa chinanso chikhoza kukhala kukula moyo wovutika. Anthu ena amangozolowera mavuto moti munthu akawachitira chinachake chabwino amasowa chochita. Musadandaule, mukhoza kuomba m’manja mitima yanu ikabwereramo!” Pulofesa wa Parro to lo gy, wa Ph.D ya Parro to lo gy komanso mkonzi wa nyuzipepala ya Daily Parro try uja anaimiriranso n’kuimba mavesi angapo m’buku lija. Koma nduna ija inaoneka kuti sinasangalale ndi mmene anthuwa anajijirikira poimba nyimboyo, moti inawauza kuti akhale kaye pansi, aimbabe. “Pofika pano, ngakhale mukanakhala kuti ndi inu amene muli nkhalapakati wa ogwira ntchito ndi oyendetsa kampaniyi, mukanaona kuti mavuto onse omwe analipo athetsedwa. Kungoyambira lero, munthu aliyense amene adzapange sitiraka kulimbana ndi kampaniyi ndiye kuti akulimbana ndi boma. Kuputa kampani imeneyi n’chimodzimodzi kutenga chala n’ku- matokosa chipani cholamula mumphuno. Kutukwana kapena kunyoza kampaniyi n’chimodzimodzi kunyoza dziko lathu, zomwe zingatanthauzenso kuti akunyoza inuyo. Kuchita zime- nezi ndi kugenda kupolisi chamba chili m’thumba.” 170