Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 170

Matigari mwachitazi. Muzigona kutali ndi moto! Kodi simuomba m’man- ja? Aa, tawaomberani m’manja akuluakuluwa kaya! Ombaninso! Bola pamenepo! Mwawaona mapepala awa? Amenewa ndi masheya. Masheyawa akupita kwa mtsogoleri wadziko lino, Pulezidenti Ole. Koma pepala limodzili ndi langa, limenelinso ndi la m asheya o m we and ipatsa. Dikirani kaye ndi malikhweru komanso miluzi yanuyo. Muchita zimenezo mukamva zonse. Kupereka masheya sikuti ndi nkhani yodabwitsa kwenikweni, izi zimachitika ndithu. Pali makampani ambirimbiri omwe achi- tapo zimenezi. Koma chosangalatsa kwambiri n’choti kampani iyiyi yaperekanso masheya ena kuchipani cholamula. Kodi mukudziwa tanthauzo la zimenezi?” “Pajatu chipani cholamula ndi chathu. Ndi chipani cha ali- yense wa ife. Ndi chipani chathuchathu. Choncho tinganene kuti kampaniyi yapereka masheya kudziko lathuli, kwa tonsefe. Kungoyambira lero, nonse kuphatikizapo amene sanakwanitse kufika pamsonkhanowu, aliyense wa inu ali ndi masheya kukampani imeneyi. Ndiyetu tinganene kuti kampaniyi ndi ya- nunso. M’mawu ena, ndi ya tonsefe. Ndi kampani yadziko lathu. Ilitu ndi boma labwino kwambiri, lomwe anthu onse ama- khala eni ake akampani, kampani kukhala m’manja mwa ali- yense! Ufulunso wodzilamulira pamenepo phi! Kodi sitinganene kuti chimenechi ndiye chikomyunizimu cha ku Africa? Kodi pangapezekenso ulamuliro woposa pamenepo amayi ndi abam- bo? Chikomyunizimu chabwino ndi chimenechi, osati chija ama- phunzitsa Karl Marx ndi Lenin, chomwe ophunzira komanso aphunzitsi apenga nacho ngati chinayamba chawapatsapo nsi- ma. Lak ini wato na cha m tem a k uni!*” *Lakini watona cha mtema kuni (Kiswahili): Kutanthauza kuti, ‘anthu amenewa ti- waonetsa polekera, tithana nawo.’ 169