Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 17

Matigari Iye anayenda molunjika kumene kunali fakitale ija ndipo kuti asasochere, ankangotsata utsi wochoka m’chumuni cha fakitaleyo. Anadutsa ofesi yotumiza makalata, siteshoni ya sitima komanso malo ena pomwe panali dzimakontena. Benz anaiona ija inamudutsanso. Kenako anakumananso ndi apolisi aja. Apolisiwo anali ataima m’mbali mwamsewu pafupi ndi chipata cholowera m’fakitale ija. Kenako apolisiwo analowa paziyangoyango penapake ngati akubisalira munthu. Bambo uja anayenda n’kumalowera komwe kunali chipata cholowera kufakitaleyo. 16