Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 168

Matigari n’kufika powachititsa ndondoli. Koma kungoti anthu akenso ndi akhwangwala. Eti amachita kudzitsekera m’chipinda n’kumaw- erenga mabuku a Karl Marx. Mukhoza kuwachotsa kaye! Mlan- du wa anthu amenewa uzengedwa pompano inu mukuona . . . Pulofesa wokhazikika wa Parro to lo gy, wa Ph.D ya Parro to lo gy komanso mkonzi wa nyuzipepala ya Daily Parro try apereka um- boni wosonyeza kuti anthu amene amaphunzitsa ziphunzitso za Marx, m’mawu ena anthu omwe amalimbikitsa chikomyuniz- imu, akuwononga ophunzira komanso ogwira ntchito anthu m’dziko muno. N’chifukwa chake anthu amenewa akufunika kutsekeredwa kaye kuti azengedwe mlandu. Si choncho pulo- fesa?” Pulofesa wa Parro to lo gy, wa Ph.D ya Parro to lo gy komanso mkonzi wa nyuzipepala ya Daily Parro try uja anaimirira n’kuimbanso mavesi atatu m’buku lija. Atamaliza anakhala pan- si, atagwirabe nyimbo zinga mwamphamvu. Kenako nduna ija inauza apolisi kuti: “Gwirani ntchito yanu!” Apolisi anayamba kukankha anthu anagwidwawo n’kuka- walowetsa m’chipinda china chomwe chinali kumbuyo kwa holoyo. 167