Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 167

Matigari m’mawu ena anthu omwe athawa kundende dzulo. Anthu ame- newa ndi amene anayambitsa mphekesera imeneyi yakuti mnge- lo Gabrieli anatsegula zitseko zandende n’kuwatulutsa. Ndikufuna ndikuuzeni zoona zake. Maso komanso makutu abo- ma ali paliponse: Kaya ndi kupolisi kaya kundende, kaya m’malo ogulitsira malonda, m’malo antchito, kusukulu, kutchalitchi, kumsika komanso ngakhale m’makoma komanso maziko a nyumba zanu. Manja athu ndi aatali kwambiri kuposa nsewu uliwonse, ndipo amathamanga kwambiri kuposa kutha- manga kwa chilopolo. Anthu amene athawawa tiwatola posachedwapa, sangakwanitse kuthawa manja a boma lathu.” Kenako atangomaliza chiganizo chimenechi, apolisi awiri analowa ndi anthu ena omwe anathawa kundende aja. Panali mlimi uja, wakuba nsima, wopha munthu, woyendayenda m’tauni, mwana wasukulu, ankafuna kuba kachikwama kan- dalama uja, wantchito anapha bwana wake uja, mphunzitsi ko- manso wamowa uja. Anthu amene ankasowa pagululi anali Giceru* komanso Matigari. *Giceru: Dzina limeneli ndi la munthu lomwenso limatanthauza ‘kazitape.’ “Mwawaona anthu amadzipusitsa kuti angathawe dzanja la boma aja? Ndi amenewotu!” Ndunayo inatero ikuloza kumene kunali anthu anagwidwa aja. “Anthu amenewa ndi amene anathawa m’ndende dzulo n’kuyamba kufalitsa mphekesera zabodza zoti mngelo Gabrieli anawatulutsa m’ndende. Iwo sanazindikire kuti makutu a boma anali momwemo. Boma likudziwa kuti a Gabrieli amenewa ndi ndani: Ndi mphunzitsi komanso wophunzira wake. Tangoganizani anthu awiri ame- newa amaphunzitsa ziphunzitso za Marx ngakhale m’ndende. Ndipo munthu ameneyu, Karl Marx wasokoneza komanso kupusitsa mphunzitsi komanso mwana wasukulu ameneyu 166