Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 166
Matigari
“Tamvetserani ndikuuzeni chinsinsi china. Boma likudziwa
kuti anthu ofuna kusokonezawa akuchita zambiri. Anthu ame-
newa apeza njira zina zosokonezera mtendere m’dziko muno.
Akumafalitsa mabodza, uvum i. Panopa pali mphekesera ina
yomwe ili ponseponse yonena kuti Khristu wabweranso. Koma
ndikufuna ndikufunseni funso: Kodi Khristu angabwere bwanji
asanaululire zimenezi ophunzira ake? Mutha kuona kuti
kutsogolo kuno kuli munthu wamulungu. Munthu wamulungu,
chonde tawauzeni anthuwa ngati mphekesera zikumvekazi zili
zoona. Kodi n’zoona kuti Yesu Khristu wabweranso?”
Wansembe uja anaimirira atakwapatira Baibulo lake.
Anayamba ndi kuyang’ana uku ndi uku ngati wakuba, chifukwa
anali asanatsimikizebe ngati zinali zoonadi kapena ayi kuti Yesu
Khristu wabweranso. Kenako anayamba kuyankhula.
“Ndikuwerenga m’buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu,
chaputala 24, kuyambira vesi 23. Likuti: ” Pomwepo munthu
akanena kwa inu: ‘Onani, Khristu ali kuno, kapena uko
musamvomereze; chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi
aneneri onama nadzawonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa:
kotero kuti akanyenge, ngati n’kotheka, osankhidwa omwe.
Onani ndakuuziranitu pasadafike.’”
Wansembe uja atangokwangula kuwerenga mavesiwa ana-
khala pansi, ndipo nduna ija inapitiriza kuyankhula.
“Mwamvatu zimene mawu a Mulungu anena! Anena kuti
tisamvere aneneri onyenga, angelo onyenga komanso a Yesu
Khristu abodza.”
“Tsopano tiyeni titembenukire pa mfundo ina. Mphekesera
yabodza imene tikunenayi inayamitsidwa ndi gulu la mbava ko-
manso zigawenga zina, gulu la anthu ophwanya malamulo,
165