Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 165
Matigari
omvera malamulofe sitinamvere malamulo a boma lomwe linka-
tilamulira, kodi mukuganiza kuti mukanakhala muli pa ufulu
lero? Muzingoyamika kuti boma lathuli likulamulidwa ndi mun-
thu wachifundo yemwenso ndi Mkhristu. Tangoganizani,
asilikali ena anatenga zida kuti alande boma. Zoona kulanda bo-
ma! Koma mitu ya anthu amenewa imagwira? Anthu amenewa
ndi oipa kwabasi chifukwa akufuna kusokoneza mtendere
umene tinaupeza movutikira kwambiri. Ali mitu gwa, ati akufu-
na kuti moto wa ufulu wawo usazime! N’chifukwa chiyani
sankachita zimenezi nthawi ya atsamunda ija? Ndiponso ana
asukulu omwe akumachita ziwonetsero panja pamaofesi a
akazembe a kumaiko a azungu, ati chifukwa choti akuthandiza
dziko la So uth Africa! Bwanji ophunzira amenewa osatengera
chitsanzo cha pulofesa wokhazikika wa Parro to lo gy? N’chifu-
kwa chiyani akulowerera za maiko ena n’kumawalamula
mmene angamagwiritsire ntchito ndalama zawo? Kaya ndi ku-
uma mitu kaya! Ziwathandiza chiyani zimenezi! Ndipo
ndikuona kuti mtsogoleri wathu, Pulezidenti Ole, ndi wachifun-
do chosaneneka ndiponso amatsatira demokalase osati
pang’ono. Kodi mukuganiza kuti zinthu zikanawathera bwanji
akanakhala m’mayiko enawa omwe satsatira malamulo? Kodi
zikanawathera bwanji akanakhala m’mayiko omwe amathana
ndi aliyense amene akuchita matukutuku kapena kuyambitsa
chisokonezo? Akanawapotokola makositu! Komanso kodi
mukuganiza kuti dzikoli likanakhala bwanji zikanakhala kuti
amene anatenga ulamuliro ndi anthu aja omwe anatenga
nkhwangwa n’kumalimbana ndi malamulo? Inde . . . dzikoli
likanamamuliridwa ndi zigawenga . . . M’mawu ena likanakhala
boma lazigawenga. Kodi zikanakhala kuti zigawengazo ndi zimene
zikulamulira dzikoli, ophunzira onse aja omwe amachita
ziwonetsero aja sakanathudzulidwa?”
164