Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 164
Matigari
amalemba nkhani zabodza, muona kuti anthu amene ankamvera
malamulo a atsamunda ndi amene anathandiza kwambiri kuti
tilandire ufulu wathu wodzilamulira. Kodi si dzulodzuloli
pamene akadaulo ophunzitsa pasukulu zaukachenjede komanso
akatswiri a Parro to lo gy anapanga msonkhano? Kodi anapeza zo-
tani? Malinga ndi kafukufuku amene anachita, anthu amene
ankagwirizana ndi atsamunda poyesetsa kuteteza lamulo ndi
amene anachititsa kuti atsamunda atipatse ufulu wathu wodzila-
mulira. Posachedwapa ndalamula kuti aphunzitsiwa komanso
akatswiriwa omwe ali ndi Ph.D ya Parro to logy akwezedwe pant-
chito komanso kuti akhale mapulofesa. Chifukwa anthu ame-
newa ndi osiyana kwambiri ndi ena aja omwe akumangoliralira
komanso kumangolongolola n’kumauza anthu kuti aukire, ati
‘ee tisinthe boma,’ komanso kumalimbikitsa mfundo zo-
sadziwika bwino zamayiko ena. Ife tikukana kuti ayi! Mapulo-
fesa awa okha ndi amene amatsatira malamulo ndiponso ku-
wateteza. Mukugwirizana nane, si choncho mapulofesa athu?”
Pulofesa wa Parro to lo gy uja anaimirira. Nayenso wina anali
ndi Ph.D ya Parro to lo gy komanso mkonzi wa nyuzipepala uja
anaimirira. Iwo anaimba mavesi atatu kuchokera m’buku lija la
Songs of a Parrot ndipo kenako anakhala pansi atagwira mabuku
awowo m’manja ngati auzidwa zoti akawasiya pansi awom-
beredwa.
Nduna ija inasangalala kwambiri ndi kuimbidwa kwa nyim-
boyo ndipo inanena kuti akapitiriza kusonyeza khalidwe
labwino ngati limenelo adzakhala pandandanda wa alendo ole-
mekezeka komanso kuti apatsidwa mamendulao monga a GKM
(Khutu la Pulezidenti) kapena MMT (Maso a Boma) .
“Ndikukhulupirira kuti mwamvetsa mfundo imeneyi
tsopano,” inapitiriza motero nduna ija. “Zikanakhala kuti anthu
163