Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 162

Matigari tsetsa kuti malamulowo akutsatiridwa. Bambo anga ndi amene anali oyamba kulimbikitsa ena kuti azimvera Mfumukazi kalekalelo. Mwina ena angadabwe: Kumvera malamulo andani? Aulamuliro wachitsamunda? Ndikufuna ndikuuzeni pano: Lamulo ndi lamulo basi. Anthu amene anazindikira mfundo imeneyi ndi amene ali anthu olozeka masiku ano. Anthu omvera malamulo ndi amene ali pamipando yonona m’dziko muno. Tiyeni tipitirizebe kumvera malamulo chifukwa malamulo ndi- wo gwero latsogolo lowala. Tadikirani ndikufotokozereni bwinobwino Mfundo imeneyi. Taonani John Boy ali apayu. Iyeyu ndi ineyo tinapitira limodzi kusukulu. Si choncho John Boy? Tinayamba ndi kupita ku Fort Hare ku South Africa. Tinalinso limodzi ku Britain. Kodi ukukumbukira zimene tina- phunzira ku Islington? Tinakupatsa dzina lakuti ‘Chilombo cha Mabuku’ chifukwa nthawi zonse unkangokhalira kuwerenga. Wakumbukira? He-he-he!” “Kodi nawenso ukukumbukira kuti anzako anali ana a mafu- mu monga Kabaka komanso Cerere Khama?”Anatero John Boy, ndipo pa nthawiyi n’kuti pakamwa pake pataphwasukiratu ndi chimwemwe kuchokera khutu ili kukafika linali. “Ife tinaku- patsa dzina loti ‘Mr Style’ chifukwa unkachita chilichonse mwa Style*. Ukukumbukira zimene tinamuchita loya Goan yemwe ankaso- wetsa anthu chonena ndi nkhani zonena za Lenin, Trotsky ko- manso Stalin? Kodi ukukumbukira mmene tinamutsekera pa- kamwa titamuuza kuti—” *Style: Kuchita zinthu motsogola, mwaushasha. “Ndine wa ku Africa ndipo ndimanyadira kulamuliridwa ndi boma lademokalase!” nduna ija ndi John Boy anayankhula mawuwa nthawi imodzi ngati akuimba nyimbo. Kenako onse anafa nawo nseko anthu ena aja akungoonerera. 161