Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 161
Matigari
Kunja kunali kusakudziwikabe kuti kukufuna kukhale nyen-
go yanji ndipo ndi mmenenso muholoyi munalili. Simunkaten-
tha komanso simunkazizira. Anthu omwe anali m’holoyo
ankayankhula mong’ung’udza ndipo sankasonyeza kuti
akondwa kapena akwiya. Magetsi nawonso sankawala
kwenikweni ndipo munali kamdima ndithu. Palibe chomwe
chinkaoneka bwinobwino.
Aliyense ankangodikirira.
Wansembe anatsegula msonkhanowu ndi pemphero: “Atate
wathu wakumwamba, tsogolerani mtumiki wanuyu, Nduna
Yoona Zachilungamo, kuti achite mogwirizana ndi chifuniro
chanu. Ambuye, khazikitsani pansi mitima ya oyendetsa fakitale
komanso ogwira ntchito, kuti akhutire ndi chigamulo chomwe
chiperekedwe pano motsatira chilungamo chenicheni.”
Pempherolo litangotha, bwanamkubwa watauniyo anadzut-
sa nduna ija kuti iyankhule ndi anthu ake. Kenako ndunayo
inadzuka n’kuyamba kutokota.
“Ndikufuna ndiyankhule mosapita m’mbali pano. Ndiyank-
hula choonadi komanso chilungamo chosatsira mchere. Ndine
mzati wa bomali. Ndine mzati wa anthu onse. Ndili ngati ku-
wala m’dzenje lamdima. Ndine nyale yachitukuko. N’chifukwa
chiyani ndanena zimenezi? Chifukwa popanda kutsatira mal-
amulo, choonadi ndi chilungamo, ndiye kuti bomanso palibe,
dziko palibe, komanso mgwirizanao palibe. Kutsatira malamulo
n’kumene kumasonyeza kuti dziko ndi logwirizana. Ndipo ine
ndinakula ndikutsatira malamulo, moti ndinganene kuti mal-
amulo ndiye kudya kwanga. Ndimatsatira malamulo, ndipo
lamulo limandimvera. Ndinaphunzira zamalamulo ndipo
ndimawakhulupirira kwambiri. Ndine amene ndimateteza mal-
amulo masiku ano. Ndimapanga malamulo ndipo ndimaone-
160