Matigari
chifukwa mbali inayo inali itapisiridwa mosamala mukajekete
kamkati. Tayeyo inalinso ndi zizindikiro zachipani cholamula—
inali ndi chithunzi cha mbalame ya parro t (chinkhwe), zilembo
za KKK, komanso zilembo zoimira chipanicho. Pasuti yake pa-
nalinso kachitsulo kofiira komwe ndi kachizindikiro kachipani
cholamula. Pathumba lajekete yake panali kansalu kopukutira
thukuta ndipo kansaluko kankasuzumira ngati kaphuka ku-
chokera m’thumba lajeketelo. John Boy ndi Robert Williams ana-
khala kudzanja lake lamanja, ndipo wansembe, bwanankubwa
watauniyo ndiponso phungu wa kunyumba yamalamulo
woimira deralo anakhala kumanzere kwake. DC wachigawochi
komanso anthu ena ogwira ntchito zam’boma anakhala mbali
iliyense yomwe anasankha. Mzera wakumbuyo kwenikweni
kwa anthuwa kunakhala azungu, amwenye komanso anthu aku-
da omwe anavala mikanjo ngati oweruza milandu. Pafupi ndi
anthuwa panalinso anthu ena atatu. Wina anali mkonzi wa
nyuzipepala ya Daily Parro try. Ndipo wina anali pulofesa wo-
khazikika wa mbiri ya Parro to lo gy, ndipo wachitatu anali
mphunzitsi wa pasukulu yaukachenjede ndipo anali ndi masam-
ba monga B.Ed., MA komanso Ph.D yafilosofe komanso Par-
rotology. Anthu atatu amenewa anali ndi mabuku a nyimbo m’manja
mwawo. Mabukuwo anali a mutu wakuti So ngs o f a Parro t zom-
we zinapekedwa komanso kulembedwa ndi akatswiri ena odzi-
wa bwino kaimbidwe ka mbalame zodziwa kuimba za parro t.
Kumbuyo kwa onsewa kunaima mkulu wa apolisi. Chapakona
panali munthu wina yemwe anavala chipewa chokhala ngati cha
anthu akuba, chija chimangoonetsa maso okha ndipo ankaoneka
kuti ndi kazitape waboma. Anadzibisa chonchi chifukwa sanka-
funa kuti ena amuzindikire. Chipewacho chinali choyera ndipo
chinali ndi maboo pamene pamakhala maso komanso pakamwa
basi.
159